Bwalo lalikulu ku Lilongwe laimitsa kaye mlandu wokhudza mmwenye ndi mavenda aku Nsungwi ku Area 25.
Mavenda omwe amagulitsa zinthu za hardware ku msika wa Nsungwi akhala akudandaula kuti m’mwenyeyu, Salahudding Akbar, anatsekula bizinesi yake ya Build Free kudera lolakwika.
Loya yemwe akuimila mavendawa, a Wesley Namasala, wati anafika kubwaloli kutsatira chiletso chomwe mmwenyeyu adakatenga posumila mavendawa kuti amutsekera shop.
A Namasala ati apempha bwalo kuti lipereke mpata kuti omwe akuimila mmwenyeyu nawo akawelenge zomwe ayankha.
Komabe, a Namasala ati mmwenyeyu wasumila anthu olakwika malinga nkuti aku unduna waza malonda ndi omwe adatseka sitolo yakeyo chifukwa chochita malonda malo olakwika m’malamulo.
M’mau ake, loya yemwe akuimila a Akbar, a Wallie Ibrahim, wati ndi zoona kuti mlanduwu auimitsa kaye pofuna kupereka mpata kuti mbali zonse ziunike zikalata.
Pa 8 April 2024, unduna waza malonda udalembera kalata a Akbar kuti akhale atachoka ku Nsungwi pasanathe masiku khumi ndi anayi.
Lero, mavenda wochuluka aku Nsungwi omwe amagulitsa zipangizo za Hardware anakhamukira ku High Court ku Lilongwe kukatsatira nkhaniyi, yomwe Justice Kenyata Nyirenda ndiye akuiunikira.
#MBCDigital
#Manthu