Nduna ya zamtengatenga a Jacob Hara ati pofika December misewu ya Kenyatta komanso Mzimba yomwe akuikonza mu mzinda wa Lilongwe itsegulidwa.
Ndunayi yanena izi itayendera misewu inayi ya Kenyatta , Mzimba, Crossroads kukafika Ku Kanengo komanso mlatho wa Lilongwe.
A Hara ati pakadali pano zovuta zina zonse zomwe zinachititsa kuti ntchitozi aziimitse kaye m’mbuyomu kaamba ka kuchepa kwa mphanvu ya ndalama ya Kwacha azikonza.
Iwo ati msewu wa Mzimba omwe unali pa K9 billion wafika pa K17 billion ndipo wa Kenyatta omwe unali pa K19 billion wafika pa K35 billion.
A Hara ati cholinga chawo nchoti dziko lino likhale ndi misewu yapamwamba komanso yolimba ndipo ati sakuopa kuika ndalama zochuluka chonchi kuti izi zitheke. Iwo ati ndiokhutira ndi mmene ma kontarakita akuchitira ntchitoyi kaamba koti akutsatira ndondomeko.