Mkulu wa Illovo Sugar Malawi, Lekani Katandula, wati pofika lero, mafakitale akampaniyi ku Nchalo ndiku Dwangwa ayambiranso kupanga sugar.
A Katundula anena izi pambali pa msonkhano wa atsogoleri a zamalonda m’dziko muno umene ukuchitikira ku Mangochi.
Iwo ati ogulitsa sugar anayamba kupikula sugar mkatikati mwa sabatayi ku Nchalo ndipo lero loweruka akhalanso atayamba kupikula ku Dwangwa.
Wolemba: Justin Mkweu
Ojambula: Edwin Mushani