Katswiri wa nkhonya m’dziko muno, Alexander ‘Cage’ Likande, wamwalira m’bandakucha wa lero pangozi ya njinga yamoto yomwe inaombana ndi galimoto.
Malinga ndi zimene akunena mnzake Byson Gwayani, Likande anachita ngoziyi dzulo usiku akuchokera ku Area 36 mu mzinda wa Lilongwe kumene kunali masewero a nkhonya.
Malipoti akuti atathamangira naye ku chipatala cha Kamuzu Central kuti akalandire thandizo, iye anamwalira.
Mwambo wa maliro a Likande akhale akuwulengeza ndi a kubanja komanso adindo a bungwe loyendetsa nkhonya m’dziko muno la MPBCB.