M’modzi mwa akatswiri oyimba chamba cha amapiano, Christopher Malera yemwe amadziwika ndi dzina loti Avokado, wati anthu ayembekezere zazikulu pomwe wayimba ndi kwaya ya Great Angels komanso Ndirande Anglican Voices mu nyimbo yomwe akuitcha ‘Ululu’.
Avokado, yemwe wayimbapo ndi anamandwa pankhani yamingoli monga Billy Kaunda, Ethel Kamwendo Banda, Thocco Katimba, Shammah Vocals, Kamuzu Barracks wati chidwi chake chili potumikira ambuye kudzera mu nyimbo.
“Pakadali pano ndi kuphika nyimbo zingapo zomwe nditulutse kutsogoloku komanso akanema ake,” watero Avokado.
Atafunsidwa ngati luso lopeka nyimbo latha potsatira kuchuluka kwa nyimbo zam’mbuku zomwe watulutsa iye wati limenelo ndiye lusolo kamba koti akutha kufukulanso nyimbozi nkukhala zokoma kumvetsera.
Katswiriyu akuyembekeza kutulutsa kanema wa nyimbo ya “M’sandipitilire” lachisanu asanatulutse nyimbo ya ‘Ululu’.