Phungu wa Blantyre City South East, Sameer Suleman wapatsidwa chilango kuti asabwerenso ku Nyumba ya Malamulo kwa nthawi yonse yomwe aphungu adzakhale akukumana (Full sitting).
Pamene Phungu wa chipani cha DPP Zomba Chisi Mark Botomani wapatsidwa chilango cha masiku awiri kuti asalowe mnyumbayi kaamba koti amayankhulabe pamene wachiwiri kwa wachiwiri wa Spikala wa Nyumba ya Malamulo anawauza kuti akhale pansi.
Mpungwepungwewu unabwera pamene a Suleman anagwira pakhosi komanso kumenya khofi phungu mzawo a Mark Botomani mnyumbayi.
Ngakhale mkulu wa aphungu a chipani cha DPP, a Mary Thom Navicha, anayesela kuleletsa, a Suleman anapitilizabe kulalata mnyumbayi ndikuwakankhanso a Navicha.
Poyankhulapo, Spikalayu anati aka ndikachitatu kuti a Suleman achite chisokonezo mnyumbayi mchifukwa chake awapatsa chilango chokhwima.
Pakali pano Nyumbayi yayamba yaimitsa kaye zokambilana zake.