Mtsogoleri wakale wa bungwe la Film Association of Malawi (FAMA), a Gift Sukali, wafunira zabwino atsogoleri atsopano amene bungweli lawasankha kumene.
A Sukali ati ndi okondwa ndi kuti akuchoka pampandowu atakwaniritsa zambiri monga kuwonetsetsa kuti anthu akudziwa zazisudzo zapakanema komanso kutha kupeza phindu kupyolera mmakanemawa.
Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti utsogoleri watsopanowu ukwaniritsa masomphenya a FAMA ndi kupititsa patsogolo bungweli kuti lithe kupeza thumba loliyendetsera.
Mtsogoleri watsopano wabungweli ndi a Dorothy Kingston, mkazi wa katswiri oyimba Zeze. Iwowa akhala akutsogolera bungweli kwa zaka zinayi.