Nthambi ya Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) yatsimikizira anthu amene njala yawakhudza m’madera ovuta kufikako m’boma la Mangochi kuti ichita chotheka kuti anthu alandire chakudya.
Mkulu wa nthambiyi, a Charles Kalemba, anena izi ku Monkey-Bay kumene bungweli likutumiza chimanga kudzera pa sitima ya Ndunduma kuti akachipereke kwa anthu amene akuvutika ndi njala m’madera a mfumu yaikulu Makanjira komanso Luranga.
“Tikutumiza matumba a chimanga okwana 28,000 olemera ma kilogalamu 50 thumba lililonse ku mabanja amene akuvutika ndi njala,” a Kalemba adatsimikiza.
M’modzi mwa akuluakulu a ofesi yoona zaulimi m’bomalo, a Masautso Stanely Njolomole, ati mabanja 331,000 ndi amene akhudzidwa ndi vuto la njala ndipo pakadali pano mabanja 124,000 awafikira kale ndi thandizo la chakudya.
Olemba: Owen Mavula