Oyendetsa mwambo opereka mphotho wa Maso Awards, a Augastine Mukisi, wati pakufunika aluso alandire maphunziro apadera okhudza miyambo yamtunduwu (awards) kuti athe kumvetsetsa momwe zimayendera.
Mukisi wati ndi odabwa ndi momwe aluso ena amayankhulira, zimene zikungoonetsa kuti satha kumvetsetsa zamphotozi.
Iwo amayankhula izi anthu atawafunsa zakuchoka komanso kutha kwa chidwi pakati pa aluso ena amene sakufuna kutenganso gawo mu Maso Awards.
A Mukusi anati iwo mbali yawo yayikulu ndi kuzindikira aluso komanso kutukula luso, zimene akwanitsa kuchita muzaka zimene mwambowu wakhala ukuchitika.
Aluso monga Che Mandota, Mr Jokes, Ethel Kamwendo Banda komanso Ching’aning’ani ndi ena mwa amene chidwi pamwambo wa Maso Awards chinawachokera.