Katswiri omenya nkhonya m’dziko la England, Tyson Fury, walengeza kuti wasiya masewerowa, malinga ndi nyumba yofalitsa nkhani ya BBC.
Nkhonya yake yomaliza ya katswiriyu, amene ali ndi zaka 36, inalipo m’mwezi wa December chaka chatha pamene adagonja atatchayidwa m’masewero achibwereza ndi Oleksandr Usyk, wa m’dziko la Ukraine, amene akusungira malamba a World Boxing Association (Super), World Boxing Council ndi World Boxing Organisation.

Komatu aka sikoyamba kuti a Fury asiye zigogodo chifukwa m’chaka cha 2022 analengeza kuti sadzaseweranso mu ring atapambadza Dillian Whyte m’mwezi wa April m’chaka cha 2022, koma patangodutsa miyezi isanu ndi umodzi anayambiranso masewerowa.
Mu mbiri ya Fury, watengako lamba wa heavyweight kawiri komanso wagonjako kawiri, kufanana mphamvu ndi osewera anzake kamodzi ndi kupambana ka 34.
M’chaka cha 2015, namatetule wa nkhonyayu adadzidzimutsa anthu okonda masewerowa pamene anakong’ontha ndi kugonjetsa amene amasungira malamba a WBA (Super), IBF, WBO, IBO, komanso Ring heavyweight, a Wladimir Klitschko a m’dziko la Ukraine.