Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Religion

Tsimikizirani anthu kuti maziko onse achitukuko apindulira aliyense- Dr. Chakwera

Mtsogoleri wadziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, walonjeza kuti boma lake lionetsetsa kuti maziko onse achitukuko, amene akuchitika pakadali pano, apindulire aliyense.

Dr. Chakwera walankhula izi pazokambirana zimene wachita ndi atsogoleri azipembedzo osiyanasiyana amchigawo cha kummawa.

Polankhula ku nyumba ya boma ya Chikoko Bay ku Mangochi, Dr. Chakwera ati mwazina, boma likuika chidwi chachikulu pantchito za mayendedwe pomanga misewu yamakono, kulimbikitsa ntchito za ulimi, migodi komanso kusamalira chilengedwe pofuna kupewa ngozi zogwa mwadzidzi, zimene zikumabwezeretsa m’mbuyo chitukuko.

“Chimene tikupempha kwa inu atsogoleri a mipingo ndi chakuti muthandize pantchito yolimbikitsa anthu kukhala ndi maganizo osinthika pakachitidwe ka zinthu ndipo zonse ziyenda bwino.”

Olemba: Owen Mavula

Related posts

More action needed to fight cancer in Malawi

MBC Online

Three arrested in K22 million soybean theft

Romeo Umali

UTM calls for intensified search for missing plane

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.