Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Ekhaya, Blue Eagles akwapulana la mulungu

Ekhaya FC yati masewero omwe ikwapulane ndi Blue Eagles mundime yotsiriza mu chikho cha K20 million King Kabvina la mulungu lino, apereka danga lounika osewera komanso kuwona madera omwe afunike kukhwimitsa, mpikisano waukulu wa Supa Ligi usanayembe.

Yemwe wakhala akuphunzitsa timuyi, Moses Chavula, wati masewerowa apereka danga kwa mphunzitsi watsopano wa mkulu wa EKhaya, Enos Chatama, kuti awone osewera omwe akhoza kuwadalira mmasewero amumpikisano wa supa ligi, womwe ukuyembekezeka kuyamba mwezi wa April.

“Masewero amenewa achitika pa nthawi yomwe mphunzitsi wamkulu wakangalika kuwumba timu ya mphamvu, nde akakhala ndi mwayi owona osewera ake. Ambiri sakutipatsa mwayi oti tingapambane, koma ife takonzeka kukagonjetsa Blue Eagles yomwe anthu akuti ndi timu ya mphamvu komanso yaikulu kaamba koti siyachilendo mu supa ligi,” watero Chavula, yemwe pano ndi wachiwiri kwa mphunzitsi wa timuyi.

Naye mphunzitsi wa Blue Eagles, Eliya Kananji, wati sakunjenjemera ndi Ekhaya FC ndipo wati osewera onse omwe amadalira apezeka lamulungu lino kuti aumbudze Ekhaya.

“Simasewero ophweka kapena ovuta, koma ife ngati Blue Eagles, takonzeka kuti titenge chikho,” watero Kananji.

Ekhaya inafika ndime yotsiriza ya chikho chimenechi itagonjetsa Chatoloma Admarc 5-1 pamene Blue Eagles inagonjetsa Mbabzi United 1-0.

Chaka chino, Blue Eagles komanso Ekhaya FC asewera mu mpikisano waukulu wa Supa Ligi kaamba kopambana mpikisano wa muzigawo. Blue Eagles ndi akatwiri ampikisano wa chigawo chapakati wa Central Region Football Association pamene Ekhaya FC inapambana mpikisano wa chigawo chakummwera wa Southern Region Football Association.

 

Olemba Yamikani Simutowe

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi U-17 girls out of COSAFA Cup

MBC Online

Two die after taking alcohol on empty stomach

Jeffrey Chinawa

Ophunzira pa UNIMA akhazikitsa kampani ya luso lamakono

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.