Apolisi mu mzinda wa Zomba amanga a Andrew Banda a zaka 25 zakubadwa powaganizira kuti anagwirira mwana wazaka 12.
Ofalitsankhani wa Polisi ya Zomba, a Patricia Sipiliano, ati a Banda anamutenga mwanayo pa msika wina pamene iye amagulitsa zigege ndipo anapita naye ku malo ena ogona alendo komwe adakapalamula mlanduwo.
Anthu ena atawona izi adatsina khutu makolo a mwanayo, omwe anathamangira ku katula nkhaniyi ku Polisi.
A Banda akawonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu ogwililira.
Iwo amachokera m’mudzi wa Majanga kwa Mfumu yayikulu Kachenga m’boma la Balaka.
#MBCDigital
#Manthu