Bwalo la milandu la Magistrate munzinda wa Lilongwe lati lipitiriza kumva mulandu wa oganiziridwa kuti amafalitsa nkhani zabodza kudzera pa intaneti a Chiyanjano Mbedza, Lachiwiri pa 30 July 2024.
Bwaloli lati a Chiyanjano Mbedza akhalabe mchitokosi kufikira Lachiwiri nthawi ya 2 koloko masana polola oyimira boma pa milandu kumalizitsa ntchito yofufuza yomwe yangotsala yochepa.
A Mbedza akuwaganizira kuti pa 25 June 2024 anafalitsa uthenga wabodza pa intaneti okhudza imfa ya malemu Dr Saulos Chilima.
Powerenga chikalata cha chigamulochi mmalo mwa oweruza, a Rhodrick Michongwe, a Benaderta Kalua anati izi ndizotsutsana ndi gawo 60 la malamulo aakulu oyendetsera dziko lino.
Olemba ndikujambula: Emmanuel Chikonso ndi Thokozani Jumpha.