Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera m’mawa uno akuyembekezeka kukumana ndi atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana ku nyumba ya boma ya Chikoko Bay m’boma la Mangochi.
Pakadali pano, atsogoleri oyimira zipembedzo ayamba kufika ku zokambilanazi.
Dr Chakwera ali m’chigawo cha kummawa kumene akugwira ntchito zosiyanasiyana za boma.
Olemba: Owen Mavula