Apolisi m’chigawo chakummwera amanga Richard Herema wazaka 42, yemwe kwawo ndi ku Mozambique, pomuganizira kuti iyeyo pamodzi ndi amzake,l anathyola nyumba ziwiri ndikuba ndalama zoposa K3 million komanso foni zam’manja kudera la Thornwood ku Mulanje.
Ofalitsankhani wapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati Herema anali mgulu la mbava 40 zomwe zakhala zikuvutitsa mderalo.
Pakadali pano, apolisi akufufuza amzake a Herema omwe anathawa.
Herema amachokera mmudzi wa Mbizi, Mfumu yaikulu Nazombe ku Milanje m’dziko la Mozambique koma amakonza njinga zakapalasa zowonongeka kuno ku Malawi.
#MBCDigital
#Manthu