Katswiri komanso m’khalakale pa ndakatulo ndi kulemba nyimbo, Benedicto ‘Okoma Atani’ Malunga, wamema oyimba m’dziko muno kuti aphunzire kupewa kudya mfulumira popeka ndi kuphika nyimbo ngati m’mene amachitira malemu ‘Soldier’ Lucius Banda.
“Masiku ano chakula ndi Bubble-gum Music, [Kodi] anthu sangaphunzire kwa oimba ngati a Kachamba ngakhalenso Soja?” anadandaula a Malunga.
Kupatula ndakatuli, Okoma Atani Malunga ndi odziwika bwinonso polemba nyimbo, monga ya Billy Kaunda yotchedwa ‘Mawu angawa’ komanso ya Lucius Banda yotchedwa ‘Nthawi’.
Dipo lomwe amalandira a Malunga panyimbo limachokera ku COSOMA pa mgwirizano umene anapanga ndi oyimba ena monga Billy Kaunda.