Kuli chikondwelero ku Parish ya mpingo wa Katolika ya Nzama m’boma la Ntcheu pamene akukhazikitsa nyengo yokondwelera kuti papita zaka 125 chiyikhazikitsireni.
Malinga ndi Bambo Godno Chinkanda a pa Parishiyi, malowa, amene ali m’dera la T/A Mpando, ndi ofunikira kwambiri mu mbiri ya a Katolika komanso dziko la Malawi.
Iwo ati, mwazina, kumeneku ndi kumene kunayambira sukulu ya ukachenjede ya katolika m’chaka cha 1902.
Ma mishonale a chi katolika anafika ku Nzama m’chaka cha 1901 pa 25 July.
Iwo ati chikondwelerochi chidzafika pa chimake m’chaka cha 2026.