Apolisi m’boma la Chiradzulu atsekera mneneri wa chizimai Jessie Windo wa zaka 74 pomuganizira kuti wavulaza pothyola miyendo ya bambo wina yemwe anapita kuti akamuchiritse pomupempherera.
Wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakumpoto chakuvuma, a Edward Kabango, atsimikiza za nkhaniyi.
A Kabango ati a Windo anapalamula mlanduwu pa 16 mwezi uno m’mudzi wa Mangira m’boma la Chiradzulu komwe mneneriyu anathyola miyendo ya bambo wina wodwala pomwe amaiongola atamaliza mapemphero kuti achire.
Apolisi ati a Windo akaonekera ku bwalo la milandu posachedwa. Mneneriyu amachokera m’mudzi wa Nyandero, mdera la mfumu yaikulu Malemia m’boma la Nsanje.
Olemba: Alufeyo Liyaya.
#MBCDigital
#Manthu