Kuli khwimbi la undipondera mwana pa bwalo la Nancholi mu mzinda wa Blantyre pamene mtsogoleri wakale wa dziko llino Dr Joyce Banda akuchititsa msonkhano.
A George Nnesa, omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Mafunde, nawo alinso pa msonkhanowu.
Padakali pano, a Noah Chimpeni ndi amene akuchita zoyankhula pamene akulandila akulu akulu amene anali ku chipani chotsutsa cha DPP ku chipani cha PP.
Olemba : Blessings Cheleuka
#MBCDigital
#Manthu