Malawi Broadcasting Corporation
Africa Local News Nkhani Politics

“MALONDA AFUNIKA PA CHIPATA CHA MWANZA” – CHAKWERA

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, wati chipata cha Mwanza ndi chofunika kuti kuzikhala malonda zomwe zingathe kubweretsa chitukuko m’Bomali.

Chipata-chi ndi chatsopano ndipo amene azatsegule ndi Dr. Chakwera pamodzi mtsogoleri wa dziko la Mozambique a Felipe Nyusi.

Boma, kudzera ku bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue authority (MRA), linamanga malowa ngati njira imodzi yowonetsetsa kuti anthu sakumatenga nthawi yayitali pofuna kulowa kapena kutuluka m’dziko lino.

Mtsogoleri wa dziko la Malawi, Dr. Lazarus Chakwera.Posachedwapa, anthu ochita ntchito malonda, monga oyendetsa galimoto zonyamula katundu, akhala akudandaula zakuchedwa kwa ndondomeko zoti alowe kapena atuluke m’dziko lino.

Malo a mtundu otere-wu akugwira kale ntchito m’maboma a Mchinji komanso Dedza.

Olemba : Timothy Kateta

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

ZOMBA POLICE IMPOUNDS 18 MOTORCYCLES

MBC Online

MPUNGWEPUNGWE KUNYUMBA YAMALAMULO

MBC Online

JUDGES TO RETIRE AT 70

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.