Nyumba yowulutsa mawu ya BBC yati nduna yaikulu ya m’dziko la United Kingdom, a Sir Keir Starmer, asiya kulandira thandizo la ndalama zoti adzigulira zovala komanso magalasi a m’maso zoti adzivala akamapita ku ntchito.
Nzika za dzikolo zakhala zikudzudzula ndunayi, maka zitadziwikanso kuti a chipani cha Labour, kudzera mwa a Waheed Ali, anawapatsa a Starmer £16,000 yomwe ndipafupifupi K37 million.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wakale wa chipanichi, a Baroness Harman, anati ndi odabwa ndi izi chifukwa munthu aliyense amayenera azizigulira yekha zovala zoti adzivala akamapita ku ntchito.
Mbuyomu, a Starmer akhala akudzudzulidwanso zitadziwika kuti akhala akulandira ma tiketi a ndalama zankhaninkhani oti adzigwiritsa ntchito akafuna kukaonera mpira ulionse wa timu ya mpira wa miyendo ya Arsenal.
Olemba: Alufisha Fischer