Gulu la achinyamata a chipani cha Malawi Congress lotchedwa MCP Youth League lapereka katundu osiyana siyana kwa odwala mu chipinda chochilira amai pachipatala chaching’ono cha Area 25 ku Lilongwe.
Achinyamatawa anakonzanso pa chipatalachi.
Wapampando wagululi, a Emmanuel Thembachako, wati apereka katundu komanso kukonza pachipatalachi ngati mbali imodzi yantchito zachifundo zomwe achinyamatawa amagwira.
“Taperekanso katunduyu ndikukonzaso pachipatala pano pofuna kuonetsera utsogoleri wachipani chathu kuti umaika chisamaliro cha anthu patsogolo,” anatero a Thembachako.
Namwino oyang’anira chipinda chochilira amai pa chipatalachi, a Amina Banda, anati katunduyu athandiza odwala ambiri omwe amasowa zakudya pa nthawi yomwe ali pachipatalapa.
A Banda ayamikiranso achinyamatawa potchetcha malo ozungulira chipatalachi ndikusesa ponena kuti zithandiza odwala ndi ogwira ntchito kukhala malo aukhondo.
Wina mwa katundu yemwe apereka kwa odwala omwe anawapeza mu chipinda chochilira amai ndi monga sopo, sugar ufa komanso ndiwo za soya.