Oyimba Silvia ‘Sife’ Sande, amene amadziwika bwino ndi nyimbo yake yotchedwa Kumaloto, walimbikitsa anthu m’dziko muno kuti ngakhale atakumana ndi mavuto adzingolimbikira ndipo asamadziyerekeze ndi ena.
Iye wati anthu ambiri amene amaoneka ngati opanda mavuto nawonso amakhala akukumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana.
Chifukwa cha ichi, Sife wayimba nyimbo yatsopano yotchedwa ‘Amafukeni’ pamodzi ndi K Banton komanso Jolasto ndipo ndi yolimbikitsa anthu.
Katswiri oyimbayu anapemphanso anthu kuti asamaganize zochotsa moyo wawo chifukwa nyengo iliyonse imakhala ndi pothera pake.