Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Senegal yachita zokonzekera pa Bingu Stadium

Timu ya Senegal yachita zokonzekera zake lero pa Bingu National Stadium, pamene ikuyembekezeka kukumana ndi timu ya Malawi mawa.

Mphunzitsi wa timuyi ongogwirizira, Pape Thiaw, wati sakutengera kuti anapambana pamasewero oyamba ndipo wati waauza anyamata ake kuti adzasewere mwakuti azidzaumva kukoma mpira.

Poyankhula ndi atolankhani ku Lilongwe, mphunzitsiyu wati akudziwa kuti Malawi ili pakwawo ndipo yakonzeka kuti ikhumudwitse timuyi koma wati salola kuti anyamata ake adzagonje.

Ikamaliza kuchita zokonzekera Senegal, timu ya Malawi ikuyembekezeka kuchitanso zokonzekera pabwalo lomweli.

Malawi ili pansi penipeni pa gulu lawo opanda point ndipo  timu ya Burkina Faso ikutsogola ndi mapointi khumi pomwe timu ya Senegal ndiyachiwili ndi mapointi 7 ndipo Burundi ili ndi mapointi atatu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

IMMIGRATION DEPORTS 11 FOREIGNERS

MBC Online

Bullets secure another partner

MBC Online

Chakwera Moves in to Find Solution to Street Vending

Alick Sambo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.