Kukhala nkoke-nkoke pakati pa matimu mu mpikisano wa Champion Kabvina chaka chino pomwe ndalama zomwe matimu amalimbirana zakwera kuchoka pa K13 miliyoni kufika pa K20 miliyoni.

Omwe amathandiza mpikisanowu a King Msaiwale Kabvina omwenso ndi mwini wake wa bwalo la za masewero la Champion ku Mponela ati mpikisanowu uyamba pa 7 April ndipo udzatha pa 27 October chaka chino.
A Kabvina ati mphotho zopita kumatimu zakwezedwanso pomwe opambana adzilandira K7.5 milluyoni kuchoka pa K3.5 miliyoni, wachiwiri K3.5 miliyoni kuchoka pa K2.5 miliyoni, wachitatu K2.5 miliyoni kuchoka pa K1.5 miliyoni pomwe timu yachinayi idzalandira K1.5 miliyoni kuchoka pa K750,000.

Chikho cha Champion chinayamba chaka chatha ndipo timu ya Mighty Mukuru Wanderers Reserve ndiyo inakhala akatswiri.
Wolemba: Emmanuel Chikonso.