Nthambi yoona zolowa ndi kutukuka mdziko muno ya Immigration yalengeza zakuyambanso kwa ntchito yodinda ndikupereka ziphaso zoyendera mchigawo chakumpoto.
Malinga ndi chikalata chomwe wasayinira ndi mneneri kunthambiyi a Wellington Chiponde, kuyambira lolemba pa 29 July anthu ofuna mapasipoti tsopano atha kufika ku Mzuzu dongosolo lonse loyenerera kuti akhale ndi chiphasochi.
Nthambi ya Immigration yakhala isakudinda ziphaso zoyendera kwanthawi ndipo yayamikira anthu kaamba kakudekha kwawo panthawiyi.