Mlembi wamkuru wa mpingo wa Zambezi Evangelical a Robert Yanduya ati ndipofunika kuti abusa mu mpingowu akhale zitsanzo zabwino pautumiki wawo ati poti anthu masiku ano amalemekeza ntchito zamunthu kuposa udindo.
A Yandura anena izi pomwe mpingowu umakhazikitsa m’busa wa mpingo wa Kawale Zambezi evangelical ku Lilongwe a Duncan Ng’oma omwe posachedwapa anasankhidwanso kukhara wachiwiri kwa wapampando wa sinodi ya mpingowu.
A Ng’oma ati kubwera kwawo pampingowu kukhala kwachabe ngati satumikira bwino kudzera muntchito zawo.
Iwo alonjeza kugwira ntchito ndi nthambi zonse zapampingowu ndicholinga chofuna kupititsa patsogolo ntchito ya Mulungu. A Ng’oma atinso akudziwa kuti anthu ali ndi chiyembekezo chochuluka koma ati achilimika pa Ambuye kuti akwanilitse maitanidwe awo pampingowu.