Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Khosolo ya Lilongwe yakhazikitsa komiti yoona za bata ndi mtendere

Khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe yati ndi yodzipereka pa ntchito yolimbikitsa bata ndi mtendere m’dziko muno.

Wachiwiri kwa mfumu ya mnzinda wa Lilongwe, a Ruth Njirayafa, ayankhula izi  munzinda wa Lilongwe pamwambo okhazikitsa komiti imene akuyitcha kuti District Peace and Unity Committee imene cholinga chake ndi kulimbikitsa bata ndi mtendere munzindawu ndi madera akumidzi.

A Njirayafa anati komitiyi ithandizira kuchepetsa kusamvana kumene kumayamba kaamba ka kulimbirana malo komanso kusiyana pa zipembedzo ndi ndale.

Komishonala wa Malawi Peace and Unity Commission, a Francis Mkandawire, anati izi ndi zofunika kwambiri pa ntchito yoteteza  ufulu wa nzika zimene zili ndi kuthekera kokhala ndi dziko la bata ndi mtendere.

“Dziko lathu ndi la mkaka ndi uchi komabe sipalephera kukhala kusamvana, ndi chifukwa chake tikuyenera kugwirana manja pa ntchito yolimbikitsa mtendere  kuti tikhale ndi Malawi wokomera aliyense,” a Mkandawire anaonjezera.

Izi zikudza pamene dziko lino likuyembekezera kuchititsa zisankho zapatatu m’mwezi wa September chaka cha mawa.

 

Olemba: Thokozani Jumpha

Related posts

Salima farmers fight back against Climate Change

Romeo Umali

Education ministry to intensify audits in private universities

Rabson Kondowe

Bus ya Bullets yachotsedwa ku khothi

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.