Katswiri ochita zisudzo m’dziko muno Jamil Chikakuda ndipo amatchuka ndi dzina loti Che Mandota wati mphoto ya MBC Entertainers of Year ndiyo ya phindu kuposa mphoto zomwe wakhala akulandira zaka za m’mbuyomu.
Che Mandota anapambana mphoto ya ochita zisudzo wapamwamba makamaka nthabwala posangalatsa anthu chaka chatha pa mphoto za asangalatsi zomwe a MBC anakonza kumathero achaka.
Iye anati mphoto zambiri sizikhala ndi phindu kwenikweni ndichifukwa chake abwera ndiganizo losiyira ena aluso.
“Ndisaname pa mphoto zomwe ndinalandira, mphoto ya MBC ndiyo inali ndi phindu kaamba koti inatisamala ngati aluso,” iye anatero.