Malawi Broadcasting Corporation
News

President Chakwera wafika ku Lilongwe kuchokera ku Blantyre

President wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafika ku Lilongwe, kuchokera ku Blantyre komwe anapita kukatsekulira chionetsero chazamalonda.

Pofika pa bwalo la ndege la Kamuzu International ku Lilongwe, President Chakwera analandiridwa ndi Mlembi wamkulu mu ofesi ya prezidenti ndi nduna zake, a Colleen Zamba ndi akuluakulu ena.

Dr Chakwera anaoneranso magule amene anavina amayi a zipani za Malawi Congress ndi UTM.


Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

University selection list out

Tasungana Kazembe

‘TIPEMPHERERE MVULA’ — EAM

Romeo Umali

Khothi laimitsa kaye mlandu wa mmwenye ndi mavenda aku Nsungwi

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.