Phungu wa Dera la Nsanje Lalanje, wayamikira boma pobweretsa chitukuko cha nyumba ya ma kompyuta pa sukulu ya Phokela CDSS mderalo.
Phunguyi, a Gladys Ganda, amayankhula izi pa mwambo otsegulira ntchito yomanga nyumbayo Lamulungu m’boma la Nsanje.
Iwo anati chitukukochi chitha kupititsa patsogolo maphunziro m’bomali chifukwa chidzapereka chidwi kwa ophunzira ambiri kuti adzipita kusukulu.
“Internet idzathandizanso anthu okhala mozungulira kutsatira zinthu zomwe zikuchitika m’dziko muno komanso kudziwa zamalonda,” a Ganda anatero.
Mkulu oyang’anira za ma computer ku Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA), a Steven Perete, anati ndi cholinga cha bungwe lawo kuchepetsa kusiyana komwe kulipo pakati pa anthu okhala mmatauni ndi akumidzi pa nkhani yogwiritsa ntchito ma kompyuta ndi zipangizo za dijito.