Bungwe loona za chisankho mdziko muno la MEC lati anthu amene akuyembekeza kuponya voti pa chisankho cha makhansala ku Mwasa Ward m’boma la Mangochi ndi Chilaweni Ward m’boma la Blantyre, akhala akulembetsabe ndi kutsimikiza maina awo mu kaundula kuyambira lolemba lapitali pa 10 June 2024, ngakhale dziko lili mu nyengo yachisoni.
Ntchito ya kalembera ndi kutsimikiza kaundulayo ikuyembekezeka kutha mawa pa 16 June.
Malinga ndi komishonala wa MEC Dr Emmanuel Fabiano, kalendala ya ndondomeko ya chisankho chapaderacho siinasinthe poti chidzachitika pa 23 July 2024, nyengo yokhuza maliro itadutsa.
“Anthu opitilira 25 percent aona kale maina awo ndipo ena alembetsa chitsegulireni kaundula pa 10 June. Tili ndi chikhulupiliro kuti pofika mawa pa 16 June anthu akhala akupitabe kukaona ngati maina awo ali mukaundula, kapena ngati akufuna kulembetsa koyamba atha kutero,” anatero a Fabiano.