Bungwe loyendetsa chisankho mdziko la South Africa mawa lamulungu lilengeza zotsatira zonse zotsimikizika zachisankho pomwe latsala pang’ono kumalizitsa ntchito yowerengera mavoti.
Pakadali pano, chipani cholamula cha African National Congress (ANC) chikutsogola ndi mavoti oposa 41 pa 100 aliwonse omwe awerengedwa, motsatana ndi Democratic Alliance (DA) ndi 21% pomwe cha mtsogoleri wakale a Jacob Zuma, uMkhonto weSizwe (MK) ndichachitatu ndi 13% ndipo Economic Freedom Fighters (EFF) chotsogoleredwa Julius Malema ndi chachinayi ndi 9%.
Malipoti akusonyeza kuti ngati chipani cholamula cha ANC chikanike kupeza 50% ya mavoti, chikuyenera kuchita mgwirizano ndi zipani zina kuti chithe kusankha mtsogoleri wadziko, malinga ndi malamulo.
Malamulo adzikolo amati chipani chomwe chadutsa theka la aphungu anyumba yamalamulo pamavoti ndicho chimakhala ndi mphamvu yosankha mtsogoleri wadziko.