Nduna yazofalitsa nkhani yalengeza kusintha kwina kwa ndondomeko ya momwe mwambo wa maliro a Dr Saulos Chilima uyendere.
Mwa zina, a Kunkuyu ati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera atsogolera mwambo wotenga thupi la Dr Chilima ku nyumba ya chisoni nthawi ya 1 koloko masana ndipo akakhala nawo pa ulendo opita ku tchalitchi ya St. Patrick’s ku Area 18 ku Lilongwe, komwe kukakhale mwambo wa mapemphero.
Malinga ndi a Kunyuyu, kuchoka ku tchalitchi thupi la Dr Chilima likakhala kunyumba kwawo ku Area 12, malinga ndi pempho la akubanja ndipo akakhala kumeneko mpaka loweruka mmawa.
Loweruka, Dr Chakwera akatsogolera mwambo wotenga thupi la Dr Chilima kupita nalo ku nyumba ya Malamulo komwe kukakhale mwambo wa mapemphero ndipo anthu osiyanasiyana akakhala ndi mwayi opereka ulemu otsiriza kwa Dr Chilima.
Thupi la Dr Chilima likakhala kunyumba yamalamuloyi mpaka lamulungu mmawa, komwe mtsogoleri wa dziko lino akatsogolerenso mwambo otenga malemuwa kupita ku Bingu National Stadium, kumene anthu akakhale ndi mwayi opereka ulemu kwa wachiwiri Kwa mtsogoleri wa dziko linoyu.
Kuchoka uko, thupi la Dr Chilima akalitengera kumudzi kwawo ku Nsipe komwe akaliyike mmanda lolemba.
Pa msonkhano wa atolankhaniwu, a Kunkuyu ati agwiritsa ntchito zina zomwe zikulembedwa mmasamba a mchezo mukafukufuku yemwe akuchitika koma apempha onse omwe ali ndi uthenga osiyanasiyana kuti apite nawo kwa anthu oyenera mmalo mopita nawo mmasamba a mchezo.
Iwo apemphanso anthu osiyanasiyana omwe akuyankhula zosiyanasiyana kuti asatengelepo mwayi opanga ndale pa maliro a Dr Chilima.
Iwo atsindika kuti kubanja ati sakufuna kuti pa malirowa pakhale za ndale.