Mbava zitatu ku Phalombe zinapempha khothi kuti liwapatse chilango chofewa kaamba koti tsiku lomwe zinagwidwa anthu mderalo anazimenya kwambiri mpaka imodzi mwa mbavazo anayigulula mano awiri.
Mneneri wapolisi ku Phalombe, Jimmy Kapanja, wati atatuwo ndi Nyadani Mandevu wazaka 39, wa m’boma la Zomba, Kingsley Mulotiwa wazaka 22 ndi Eric Muwawa wazaka 26, awiriwa ochokera kwa Namasoko ku Phalombe.
Malinga ndi a Kapanja, mbavazo, zomwe zinali ndi zida zowopsa kuphatikizapo zikwanje, zinathyola nyumba ziwiri m’bomalo ndikuba njinga zamoto ziwiri ndi ndalama pafupifupi K1 million ndikuthawa.
Patadutsa masiku angapo, apolisi anagwira mbavazo ndipo zitakaonekera kukhothi, zinapempha chilango chofewa koma woweruza milandu sanamvere izi moti zikakhala ku ndende zaka 8 aliyense.