Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani Sports

Thandizani mpira wa m’maboma — CRFA

Bungwe la Central Region Football Association (CRFA) lapempha anthu okonda mpira wa miyendo m’dziko muno kuti abwere poyera ndikuthandiza mpira wa m’maboma.

Mlembi wamkulu wa bungweli, Antonio Manda, anati m’maboma muli achinyamata aluso kwambiri koma sakhala ndi mwayi oti apite patsogolo kaamba kosowa mipikisano.

A Manda anayankhula izi pamwambo okhazikitsa chikho cha ndalama zokwana K2.5 million chotchedwa By Grace Football m’boma la Ntcheu.

M’busa McLean Chimwenje ndiye adayikapo ndalamazi ataona kuti m’boma la Ntcheu muli achinyamata ambiri amene amasowa zochita komanso kufuna kufalitsa uthenga wa Mulungu.

A Clement Mafula, amene ndi mlembi wa bungwe loyendetsa mpira wamiyendo m’bomali, anayamikira ndalama zimene aziyika m’chikhochi, ndipo anati kwa nthawi yayitali akhala akudalira anthu a ndale kuti akhazikitse zikho.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CHAKWERA HOMEBOUND

MBC Online

MAIIC yapanga phindu lokwana K2.5 billion mu 2023

Justin Mkweu

ROSAF embarks on road safety awareness campaign

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.