Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Khonsolo ikufuna ndalama za chitukuko zidzibwera motsata ndondomeko

Akuluakulu a khonsolo ya m’boma la Nkhotakota ati kulandira kwa ndalama  zachitukuko mopelewera komanso mopanda ndondomeko  kukusokoneza  magawo ambiri akagwiridwe kawo kantchito m’bomali.

DC wa bomali, a Ben Matengeni Tonho, wanena izi Ku nyumba ya malamulo  pomwe  komiti yoona za maboma aang’ono komanso   chitukuko cha mmidzi inawayitsanitsa kuti akamve mavuto omwe akukumana nawo.

Iwo ati akhala akukumana ndi mavutowa kuyambira m’chaka cha chuma cha  2023 mpaka 2024 ndipo ati akhala akuvutika kugula zinthu zofunika pa khonsolo, kulipira ma khansala komanso kulipira ma bilu, mwa zina.

Wapampando wa komitiyi, a Horace Chipuwa, yemwenso ndi phungu wa Lilongwe Mapuyu, watsimikizira khonsoloyi  kuti apititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

CS-EPWP improving livelihoods of participants in Nkhata Bay

MBC Online

MCCCI Business Leaders Summit receives boost from Britam Insurance

Alinafe Mlamba

SCIENCE BACKS SMOKE-FREE PRODUCTS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.