Malawi Broadcasting Corporation
Africa Development Local Local News Nkhani

Achinyamata asamalire okalamba — Mayi Mbambande

“Achinyamata asinthe maganizo awo poona anthu okalamba ngati mfiti,” izi ndi zimene anayankhula Deborah Mbale, mwini wake wa Mayi Mbambande, malo amene amasamalirako anthu okalamba.

Iye wanena izi pamene amalandira thandizo landalama zokwana K1 million kuchokera ku kampani ya Chisurija Transportation Services (CTS).

Jaquelin Bokosi, amene ndi mwini wa kampaniyi CTS, wati anaganiza zopereka thandizoli kaamba kakuti malo a Mayi Mbambande akugwira ntchito yobweretsa chimwemwe kwa anthu achikulire.

A Nasitima Chikadwala, omwe ndi m’modzi mwa anthu okalamba zedi omwe akukhala pa malopa, anati malowa, omwe ali m’mudzi wa Dzama kwa Mfumu yaikulu Chitukula ku Lilongwe, anawachotsa chitonzo chifukwa iwo akusamalidwa.

Padakali pano, malowa akuyang’anira anthu okalamba okwana 85.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chitimba Communities demand action on delayed Water Supply Project

Rudovicko Nyirenda

Mavuto ndiwo akulimbikitsa mchitidwe odzipha- Chiluzi

Paul Mlowoka

Adzudzula zipani zomwe zikufuna kuti MEC isagwiritse chiphaso cha unzika pazisankho

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.