Malawi Broadcasting Corporation
Local News Sports

Tiloreni final ikakhale akalambula bwalo a Silver ndi Wanderers — Migogo

Mtsogoleri wa masewero mpira wamiyendo wa amayi m’dziko muno, Adelaide Migogo, wapempha bungwe la Super League kuti liyike masewero a Silver Strikers ndi Mighty Wanderers pabwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe Lamulungu likudzali.

Iwo ati sakufuna kugawanitsa anthu otsatira masewero mu mzindawu popeza kulinso masewero otsiriza amumpikisano wa Goshen FAM Women’s Championship pabwalo lomweli.

Malinga ndi m’ndandanda wa masewero, masewero a ligi apakati pa Silver ndi Manoma akuyenera kudzachitika pa bwalo la Silver ku Lilongwe.

Athambitsana Lamulungu

Lero masanawa, masewero alipo mundime ya kapherachoka (quarterfinals) pakati pa Civil Service United ndi MDF Lioness komanso Silver Strikers’ Ladies ndi Ascent Academy.

Olemba: Praise Majawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

US Army Maps Malawi to Aid Government’s Decision-Making

Yamikani Simutowe

Awanjata pogulitsa mankhwala owopsa

Blessings Kanache

CFTC tackles contractual matters in Consumer Rights commemoration

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.