Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local News Nkhani

Athana ndi umphawi pokonza sopo

Amayi anayi ochokera kwa Gavi m’dera la mfumu Kapeni m’boma la Blantyre akupha makwacha atatsekula bizinesi yawo yopanga sopo pofuna kuthana ndi umphawi.

Amayiwa adachita izi atalandira ndalama ku bungwe la Community Savings and Investment Promotion (COMSIP) ndipo adasonkherana ndi kugula zipangizo zogwilira ntchitoyi, imene idayamba m’mwezi wa August chaka chatha.

Sopo amene akukonza

A Agnes Bamusi, m’modzi wa amayiwa, anati iwo padakali pano akupanga sopo 1000 pa tsiku yemwe m’modzi amamugulitsa pa mtengo wa K200.

“Tikagulitsa sopoyu pamwezi timagawana phindu la ndalama zosachepera K20,000 ali yense ndipo kuchokera ku ndalamazi aliyense mwa ife timachita bizinesi zina payekha,” a Bamusi anafotokoza.

Kuonetsa m’mene amachitira

Amayiwa analandiranso thandizo la ndalama zogulira zipangizo za ulimi kubungwe lomweli pansi pa ntchito ya LESP ndipo akuti athana ndi vuto la njala.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mzuzu mass grave trial stalls as defendant fails to appear

MBC Online

Scholarship for girl with albinism

Blessings Kanache

FUTURELIFE- NOW! AWARDS BEST STUDENTS IN DEDZA

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.