Malawi Broadcasting Corporation
Development Local News Nkhani

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yagumula sitolo zoposa 60 mkatikati mwa Lilongwe

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe m’mbandakucha walero wagwetsa ndi kugumula nyumba zoposa 60 zogulitsira katundu ntauni ya munzinda wa Lilongwe kamba koti eni ake anazimanga mosatsata malamulo.

izi zikudza pomwe unduna wazamalo posachedwapa walengeza zoyamba ntchito yogwetsa nyumba zomwe zamangidwa mosatsata mapulani.

Arfoso Zudu Jamali, m’modzi wa eni nyumba azigumulazo, adandaula ponena kuti chenjezo linali la masiku 29 ndipo agumula masikuwa asanakwane.

A Jamali ati mashopu osankhika ndi omwe awagumula kusiya ena omwe akuti ndi anzika za maiko ena.

Wachiwiri kwa wapampando wa eni ma minibus, a Heirman Msowoya, ati iwo avomereza zomwe undunawu wachita kaamba koti anawapatsa chenjezo asanayambe ntchito yomanga pamalopo.

 

Related posts

Late header sinks Wanderers

Romeo Umali

Project M marks one year of promoting Malawi through positive stories

Alinafe Mlamba

TNM Super League mid-season Analysis

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.