Malawi Broadcasting Corporation
Entertainment Entertainment Local Local News Nkhani

Masamba ndi mtsogoleri wa ochita zisudzo

Louis Masamba ndiye amusankha kukhala mtsogoleri wa National Theatre Association of Malawi (NTAM).

Izi zikudza pamene anthu ochita zisudzo oposa 300 anasonkhana m’boma la Salima kuti akasankhe adindo oyendetsa bungwe lawo.

Masamba, amene amapikisana ndi Harriet Kanyenda, wapeza mavoti 275 ndipo Kanyenda wapeza 22.

“Ambuye alemekezeke pondilora kuti nditsogolere bungwe la zisudzo m’dziko muno,” Masamba anatero.

Wapampando yemwe anayendetsa chisankhochi, a McArthur Matukuta, anati ndi okondwa kuti zonse zatha bwino.

“Opikisana anakonzekera mokwanira,” a Matukuta anatero.

Amene anayimilira boma kudzera ku unduna oona zachikhalidwe, a James Thole, analangiza anthu amene asankhidwawo.

“Muli ndi ntchito yayikulu yakuti mukonze malamulo aakulu a bungwe lanu,” a Thole adafotokoza.

Wachiwiri kwa a Masamba, amene adali wapampando wa azisudzo a chigawo chakummwera komanso mtsogoleri wa gulu la Logos Theatre, ndi a Sam Sambo.

A Precious Denja atenga udindo wa mlembi, achiwiri awo ndi a Mildred Namwaza Banda.

Msungichuma ndi a Shadreck Jumaina, ofalitsankhani ndi a Gibson Chisale ndipo achiwiri awo ndi a Macxyitings Mdoka.

Masamba watenga udindowu kuchokera kwa a Max Chiphinga amene sadapikisane nawo atatsogolera bungwe la anthu azisudzowa kwa zaka zitatu.

Olemba: Stanley Kadzuwa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chakwera advises acting Justices to keep composed temperament

MBC Online

Children urge authorities to Address challenges in Dedza

Sothini Ndazi

Alimi olimbikira akondweretsa mayi Mia

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.