Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local Nkhani

TCM yachenjeza aphunzitsi osapezeka m’kaundula wawo

Bungwe la Teachers Council of Malawi (TCM) lati pofika pa 1 April chaka chino lamulo ligwira ntchito kwa aphunzitsi amene sapezeka mu kaundula yemwe bungweli likuchititsa.

Aphunzitsiwa ndi a sukulu za mkombaphala, pulayimare, sekondare komanso ophunzitsa aphunzitsi.

M’modzi mwa akuluakulu ku unduna wa za maphunziro, Professor Golden Msilimba, ndi amene anena izi pa msonkhano wa olembankhani munzinda wa Lilongwe.

A Msilimba ati pakadalipano aphunzitsi oposa 93,000 ndi amene akufuna kulembetsa m’kaundulayu ndipo 42,000 akufuna ziphaso.

56,000 mwa iwo akufuna kulembetsa kugwiritsa ntchito mapepala ndipo 37,000 akufuna kulembetsa kudzera pa makina a internet.

Mkulu wa TCM, a Grace Mphandamkoko, ati kuchuluka kwa aphunzitsi ofuna kulembetsa pa mapepala kwachulutsa ntchito ya bungweli chifukwa aphunzitsi ambiri a pulayimare omwe anaphunzira zaka zam’mbuyomu sakudziwa kugwiritsa ntchito ndondomeko za luso la makono.

Komabe, a Msilimba anatsindika kuti unduna uchilimika kuphunzitsa aphunzitsi oterowa kudzera mu ndondomeko ya Continuous Professional Development kuti athe kuthandiza aphunzitsi omwe sakutha kugwiritsa ntchito njira za makonozi.

Related posts

Blantyre 42.195 km race set for September

MBC Online

Govt pledges completion of 12,500 security houses

MBC Online

Elderly man jailed for indecent assault

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.