Malawi Broadcasting Corporation
Environment Local Local News Nkhani

‘Kulimbikitsa ukhondo ndi udindo wa tonse’

Bungwe la IsraAID lapempha ochita malonda mu msika wa Mbayani ku Blantyre kuti adzikhala a ukhondo n’cholinga chakuti apewe kufala kwa matenda monga Cholera.

Mkulu wa bungweli, a Apio Annet, ndi amene anapereka langizoli pamene iwo, pamodzi ndi anthu ena amasesa mu msikawu ngati chimodzi mwa zinthu zochitika pa tsiku la World CleanUp Day, limene limalimbikitsa zosamala malo kuti akhale aukhondo.

A Annet anati kukhala pa malo aukhondo ndi koyenela komanso kofunika kuti aliyense atengepo mbali posamalira malo amene amakhala.

IsraAID mogwilizana ndi Green Girls Platform ndi amene anapereka zipangizo zothandiza kulimbikitsa ukhondo pa msika wa Mbayani.

Bungweli linayamba ntchito zake m’dziko muno chaka chatha ndipo lakwanitsa kuthandiza anthu kukhala ndi madzi aukhondo m’ma boma a Mulanje ndi Phalombe pokonza mijigo yoposa 100.

Related posts

Five nominated in Rainbow Paints Netball player of the tournament

Romeo Umali

CHAKWERA ENGAGES SOUTHERN REGION CHIEFS IN DEVELOPMENT DIALOGUE

MBC Online

COFO donates medical supplies to Chikwawa District Hospital

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.