Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

Osakhala, kuchita malonda pafupi ndi njanji — Boma

Boma lati anthu okhala komanso ochita malonda kufupi ndi njanji ali ndi udindo oteteza zipangizo za njanji kuti ntchito za sitima zipite patsogolo m’dziko muno.

Malinga ndi malamulo, anthu akuyenera kuchita malonda komanso kukhala pa mtunda wa ma mita 45 otalikirana ndi njanji.

Nduna ya za mtengamtenga, a Jacob Hara, ndi amene anayankhula izi Lamulungu ku ofesi za boma munzinda wa Lilongwe pokonzekera sabata yolimbikitsa chitetezo komanso kufunika kotsatila malamulo a njanji ya sitima.

A Hara anati ndi zokhumudwitsa kuti anthu ena akuwononga komanso kuba zitsulo za njanji, zimene anati zikuyika miyoyo ya anthu pachiwopsyezo komaso kusokoneza ntchito za malonda m’madera zimene zimadalira sitima yapa njanji.

Iwo analimbikitsanso anthu akuti akhale patsogolo kuteteza njanji komanso kuneneza ku police za anthu amene akuba komaso kuwononga njanji m’dziko muno.

M’chaka cha 2019, mabungwe aku m’mwera kwa Africa amene ali pansi pa Southern African Railway Association anagwirizana kuti adzikhala ndi sabata yolimbikitsa chitetezo cha njanji komanso anthu m’madera amene kumadutsa sitima.

Izi zimayenera kumachita chaka ndi chaka mwezi wa October, koma kuno ku Malawi izi zichitika kuyambila Lolemba pa 18 November mpakana pa 24 November 2024 m’boma la Salima pansi pa mutu wakuti ‘Kondani Moyo Wanu, Lemekezani Sitima’.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

UK supports Malawi’s education sector with K90BN

Olive Phiri

NGO steps in to assist hunger-stricken families in Balaka

MBC Online

Burning Spear abwera ku Malawi mu October Kudzaimba

Emmanuel Chikonso
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.