Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Adakali mu ululu

M’modzi mwa oyimba nyimbo zauzimu m’dziko muno, Peter Uyu Mlangeni, adakali mu ululu kutsatira ngozi ya galimoto chaka chatha m’mwezi wa September.

M’modzi mwa anzake a Mlangeni, Norman Phiri, ndi amene wanena izi ku Lilongwe pomwe watinso kutsatira mavuto omwe oyimbayu akukumana nawo, oyimba nyimbo zauzimu akonza phwando la maimbidwe lomwe ati lidzachitikira ku Sheaffer ku Lilongwe kuti apeze ndalama zoti zithandizire kugula mankhwala komanso zithandizire moyo wake wa tsiku ndi tsiku.

 

Malinga ndi a Phiri, oyimba ambiri auzimu adzipereka kudzaimba mwaulere ndipo ati ndalama zonse zomwe zidzatoleredwe zidzaperekedwa kwa Mlangeni.

Phiri wapemphanso anthu kuti adzabwere ku phwandoli, lomwe ati lidzayambe mmamawa mpaka madzulo pa 8 July, lomwe lidzakhale la tchuthi chokondwerera ufulu odzilamulira.

Related posts

Chakwera hails Israel on labour export deal

Mayeso Chikhadzula

Invest in innovation — LUANAR

Romeo Umali

MCP lauds late Chaziya’s son for development projects

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.