Phungu wa dera lakummawa kwa boma la Rumphi, a Kamlepo Kalua, ayamikira mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, chifukwa cholora bungwe la MACRA kuti limange chipinda chatsopano chophunzitsira luso la computer pa Sukulu ya Jalawe CDSS.
Kalua wayankhula izi pamene bungweli limakhazikitsa ntchitoyi ku Rumphi.
Iye anati chitukukocho chibwera limodzi ndimagetsi pasukulupo ponena kuti makina a computer amafuna magetsi ndiye sizingatheke kuti ayike makinawa pamalo pamene palibe magetsi.

Bungwe la MACRA likumanga zipinda zophunzitsira makina a computer musukulu 75 za m’dziko muno, ntchito imene ikuyembekezeka kutha m’miyezi itatu ikubwerayi ndipo igwilitsa ntchito ndalama zokwana K6 billion.
Olemba: Hassan Phiri