Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

SILVER STRIKERS YASAYINA OSEWERA WACHITATU TSOPANO

Timu ya Silver Strikers yasayina amene anali osewera kutsogolo kwa timu ya Dedza Dynamos, Charles Chipala, pa mgwirizano wa zaka zitatu.

Chipala wasewereraponso matimu monga Michiru Madrid, Zomba United ndi ena amdziko la Mozambique m’mbuyomu.

Uyu ndi osewera osewera oyamba kubwera kutimu ya Silver Strikers pansi pamphunzitsi watsopano Peter Mponda ndipo ndiwachitatu potsatira kubwera kwa  Christopher Gototo ndi McDonald Lameck ku timuyi kuchokera kutimu ya Blue Eagles.

Wolemba Emanuel Chikonso

Related posts

Mbadwa zokhudzika zakana zionetsero za Malawi First

Rabson Kondowe

Dr Chakwera adzudzula anthu opondereza pa ntchito ya mtukula pakhomo

Romeo Umali

Aliyense atenge gawo posamala misika — Khonsolo ya Lilongwe

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.