Timu ya Silver Strikers yasayina amene anali osewera kutsogolo kwa timu ya Dedza Dynamos, Charles Chipala, pa mgwirizano wa zaka zitatu.
Chipala wasewereraponso matimu monga Michiru Madrid, Zomba United ndi ena amdziko la Mozambique m’mbuyomu.
Uyu ndi osewera osewera oyamba kubwera kutimu ya Silver Strikers pansi pamphunzitsi watsopano Peter Mponda ndipo ndiwachitatu potsatira kubwera kwa Christopher Gototo ndi McDonald Lameck ku timuyi kuchokera kutimu ya Blue Eagles.
Wolemba Emanuel Chikonso